Wokondedwa Ambuye Yesu,
Bwerani mu mtima mwanga.
Ndikhululukireni machimo anga.
Ndisambitseni ndi kundiyeretsa.
Ndimasuleni.
Yesu, zikomo Inu kuti munandifera ine.
Ine ndikukhulupirira kuti Inu mwauka kwa akufa.
Ndi kuti Inu mukubweranso chifukwa cha ine.
Ndidzazeni ndi Mzimu Woyera.
Ndipatseni chilakolako cha otayika.
Njala ya zinthu za Mulungu.
Ndi kulimbika mtima koyera kulalikira Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu.
Ndapulumutsidwa!
Ndabadwanso mwatsopano!
Ndakhululukidwa!
Ndipo ine ndiri pa ulendo wanga wopita Kumwamba.
Chifukwa ndili ndi Yesu mu mtima mwanga.
